Psalms 82

Salimo la Asafu.

1Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;
Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

2“Mudzateteza osalungama mpaka liti,
ndi kukondera anthu oyipa?
3Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
4Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;
apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

5“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.
Amayendayenda mu mdima;
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

6“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,
nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
7Koma mudzafa ngati anthu wamba;
mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”

8Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.
Copyright information for NyaCCL